Section 01 — Eligibility
Eligibility/ Kuyenerera
English
You can request a refund if:
- The order was not delivered within the promised timeframe.
- The product is significantly different from its description.
- The item arrived damaged or defective.
- The seller/brand failed to fulfil the order without explanation.
Note: The 5% service fee is non‑refundable.
Chichewa
Mutha kupempha kubweza ndalama ngati:
- Odala sinafikire munthawi yomwe idalonjezedwa.
- Chinthucho ndi chosiyana kwambiri ndi momwe chidafotokozedwera.
- Chinthucho chidafika chili chowonongeka kapena cholakwika.
- Wogulitsa/ kampani sanakwaniritse odala popanda chifukwa.
Chidziwitso: 5% service fee sibwezedwa.
Section 02 — Exclusions
Non‑Refundable/ Zosabwezedwa
English
- Orders where the buyer changed their mind after confirmation
- Items that have been worn, washed, or altered.
- Orders placed more than 14 days ago.
Chichewa
- Ma odala osinthidwa pomwe wogula asintha malingaliro pambuyo povomereza.
- Zinthu zomwe zidavalidwa, kutsukidwa kapena kusinthidwa.
- Zinthu za digito kapena ma gift card.
- Ma odala omwe adapangidwa kupitirira masiku 14 apitawo.
Section 03 — Steps
How to Request/ Momwe Mungapemphere
English
- Log in to your Buyer Dashboard.
- Click Request Refund.
- Enter your order code, the amount you wish to claim, and the reason.
- Submit — our team will review within 24–48 hours.
You can track the status under Refund History.
Chichewa
- Lowani mu Buyer Dashboard yanu.
- Dinani Request Refund.
- Lembani nambala ya odala, ndalama zomwe mukufuna, ndi chifukwa.
- Tumizani — gulu lathu lidzapenda mkati mwa maola 24–48.
Mutha kutsata momwe pempholi lilili mu Refund History.
Section 04 — Timeline
Processing & Payout/ Kulipira
English
- Approved refunds are returned to the original payment method.
- The process typically takes 3–7 business days after approval.
- The 5% service fee is retained by fashionBello.
- If you used mobile money, the exact amount (minus fee) will be sent to the same number.
Chichewa
- Ndalama zomwe zavomerezedwa zibwezedwa ku njira yomwe mudalipira.
- Kubweza kumatenga masiku 3–7 ogwira ntchito pambuyo povomereza.
- 5% service fee imasungidwa ndi fashionBello.
- Ngati mudalipira ndi mobile money, ndalama yeniyeni (kupatula fee) idzatumizidwa ku nambala yomweyo.
Section 05 — Escalation
Disputes/ Mikangano
English
If your refund request is denied and you believe it was unfair, you can escalate to our support team. We will re‑examine the case and provide a final decision within 5 working days.
Chichewa
Ngati pempho lanu la kubweza ndalama likakanidwa ndipo mukukhulupirira kuti silinachitike mwachilungamo, mutha kutumiza ku gulu lathu lothandizira. Tidzawunikanso ndipo tidzapereka chigamulo chomaliza mkati mwa masiku 5 ogwira ntchito.