Legal & Binding

Terms of Service

The rules that keep fashionBello fair, safe, and reliable for every buyer and seller in Malawi.

Section 01 — Agreement

Acceptance/ Kuvomereza

English

By accessing or using fashionBello (the "Platform"), you agree to be bound by these Terms of Service. If you do not agree with any part of these Terms, please do not use the Platform.

These Terms apply to all visitors, buyers, sellers, and brands who access or use the Platform.

Chichewa

Mwa kugwiritsa ntchito kapena kufikira fashionBello ("Pulatifomu"), mukuvomereza kutsatira Malamulo a Ntchito awa. Ngati simukuvomereza gawo lililonse la Malamulo awa, chonde musagwiritse ntchito Pulatifomu.

Malamulo awa amakhudza aliyense amene amalowa kapena kugwiritsa ntchito Pulatifomu, kaya ndi ogula, ogulitsa, kapena makampani.

Section 02 — Accounts

Eligibility & Accounts/ Akaunti

English
  • You must provide accurate, current, and complete information during registration.
  • You are responsible for keeping your password and account confidential.
  • Notify us immediately of any unauthorised use of your account.
Chichewa
  • Muyenera kupereka chidziwitso cholondola, chapano komanso chathunthu poleka akaunti.
  • Muli ndi udindo woteteza achinsinsi a password ndi akaunti yanu.
  • Tiuzeni mwamsanga ngati akaunti yanu yagwiritsidwa ntchito mosaloledwa.
Section 03 — Transactions

Buying & Selling/ Kugula ndi Kugulitsa

English
  • Sellers are solely responsible for the accuracy of their product listings (photos, prices, descriptions, stock).
  • Buyers agree to pay the listed price plus the 5% service fee at checkout.
  • Delivery costs are the responsibility of the buyer and depend on the delivery company selected by the buyer, unless otherwise stated.
  • fashionBello is a marketplace — we do not sell products ourselves.
  • All orders are subject to the Refund Policy.
Chichewa
  • Ogulitsa ndi omwe ali ndi udindo woona kuti zinthu zomwe alemba (zithunzi, mitengo, mafotokozedwe, katundu) ndi zolondola.
  • Ogula amavomereza kulipira mtengo wolembedwa pamodzi ndi service fee ya 5%.
  • Ndalama zotumizira katundu zimakhala za wogula ndipo zimatengela kampani yotumizira katundu yomwe wogulayo wasankha, pokhapokha ngati zanenedwa mosiyana.
  • fashionBello ndi msika wokha — sitigulitsa zinthu tokha.
  • Ma odala onse amatsatira Refund Policy.
Section 04 — Money

Payments & Fees/ Malipiro

English
  • All payments are processed through secure channels on the Platform.
  • A 5% service fee is applied to every order and is non-refundable.
  • Prices are listed in Malawian Kwacha (MWK) unless otherwise noted.
  • Payouts to sellers are made after order confirmation and any applicable review period.
  • fashionBello may adjust fees with advance notice; existing orders are not affected.
Chichewa
  • Malipiro onse amachitika kudzera munjira zotetezeka zomwe zilipo pa Pulatifomu.
  • Service fee ya 5% imawonjezeredwa pa odala iliyonse ndipo siyibwezedwa.
  • Mitengo ili mu Kwacha ya Malawi (MWK) pokhapokha atanena zina.
  • Malipiro a ogulitsa amaperekedwa pambuyo pa kutsimikizira odala ndi nthawi yoyang'ana ngati ikufunika.
  • fashionBello ikhoza kusintha ma fee ndi chidziwitso cham'mbuyo; ma odala omwe achitika kale sasinthidwa.
Section 05 — Rules

Prohibited Conduct/ Zoletsedwa

English

You agree not to:

  • Sell or list illegal, counterfeit, or stolen items.
  • Commit fraud, misrepresent products, or deceive other users.
  • Abuse, threaten, or harass other users.
  • Attempt to hack, scrape, or disrupt the Platform.
  • Use the Platform for money laundering or any unlawful purpose.

Violation may result in suspension or permanent termination of your account.

Chichewa

Mukuvomereza kuti musachite izi:

  • Kugulitsa kapena kulemba zinthu zoletsedwa ndi lamulo, zonyenga, kapena zobedwa.
  • Kuchita chinyengo, kunamizira zinthu, kapena kuphwanya anthu ena.
  • Kuzunza, kuopseza, kapena kukwiyitsa anthu ena.
  • Kuyesa kulowa mosaloledwa, kukopera deta, kapena kuwononga Pulatifomu.
  • Kugwiritsa ntchito Pulatifomu pochita zachinyengo za ndalama kapena china chilichonse chosaloledwa.

Kuphwanya malamulo kungathe kuyimitsa kapena kutseka akaunti yanu mpaka kalekale.

Section 06 — Ownership

Intellectual Property/ Zolemba

English
  • All content on the Platform (logos, text, design, code) is owned by fashionBello or its licensors.
  • You may not copy, distribute, or reuse Platform content without written permission.
  • Sellers retain ownership of their product photos and descriptions.
Chichewa
  • Zonse zomwe zili pa Pulatifomu (ma logo, zolemba, kapangidwe, khodi) ndi za fashionBello kapena omwe adapatsidwa chilolezo.
  • Simungalole kukopera, kugawa, kapena kugwiritsanso ntchito zomwe zili pa Pulatifomu popanda chilolezo cholembedwa.
  • Ogulitsa amasunga ufulu wa zithunzi ndi mafotokozedwe awo.
Section 07 — Limits

Limitation of Liability/ Malire a Udindo

English
  • fashionBello does not manufacture, inspect, or guarantee any product listed by sellers.
  • We are not liable for delays, losses, or damages caused by sellers, shipping providers, or events beyond our control.
  • Our total liability to you will never exceed the service fee you paid on the affected order.
Chichewa
  • fashionBello siyipanga, siiyang'ana, kapena kutsimikizira zinthu zilizonse zomwe ogulitsa amalemba.
  • Sitiyenera kutaya ndalama chifukwa cha kuchedwa, kutayika, kapena kuwonongeka kobwera kuchokera kwa ogulitsa, onyamula katundu, kapena zochitika zomwe sitingathe kuzilamulira.
  • Udindo wathu wonse kwa inu sungathe kupitirira service fee yomwe munalipira pa odala wokhudzidwayo.
Section 08 — Changes

Modifications & Termination/ Zosintha

English
  • We may update these Terms at any time. Changes will be announced on the Platform.
  • Continued use after changes means you accept the updated Terms.
  • We may suspend or terminate your account if you violate these Terms.
  • You may close your account at any time by contacting support.
Chichewa
  • Titha kusintha Malamulo awa nthawi iliyonse. Zosintha zidzalengezedwa pa Pulatifomu.
  • Mukapitiriza kugwiritsa ntchito pambuyo pa zosintha, mukuvomereza Malamulo osinthidwa.
  • Titha kuyimitsa kapena kutseka akaunti yanu ngati mukuphwanya Malamulo awa.
  • Mutha kutseka akaunti yanu nthawi iliyonse polumikizana ndi gulu lothandizira.
Section 09 — Jurisdiction

Governing Law/ Malamulo

English

These Terms are governed by the laws of the Republic of Malawi. Any dispute arising from your use of the Platform will be resolved exclusively in the courts of Malawi.

If any part of these Terms is found unenforceable, the remaining parts remain in full force.

Chichewa

Malamulo awa amatsata malamulo a dziko la Malawi. Mkangano uliwonse wobwera chifukwa cha kugwiritsa ntchito Pulatifomu udzathetsedwa ku makhoti a Malawi okha.

Ngati gawo limodzi la Malamulo awa likapezeka kuti silingathe kutsatiridwa, magawo ena onse akhalabe othandiza mokwanira.

Section 10 — Support

Contact Us/ Lumikizanani

English

If you have questions about these Terms, please reach out:

  • Email: fashionbello265@gmail.com
  • Support page: fashionBello Support
  • Buyer Dashboard → Contact Support
Chichewa

Ngati muli ndi mafunso okhudza Malamulo awa, chonde lumikizanani nafe:

  • Imelo: fashionbello265@gmail.com
  • Tsamba lothandizira: fashionBello Support
  • Buyer Dashboard → Contact Support
Need help? Contact Support · Lumikizanani nafe